WANDERERS IKUSAKA CHIKHO CHA CHARITY SHIELD CHOYAMBA
Timu ya Mighty Wanderers ikusakasakabe chikho chawo choyamba cha Charity Shield pomwe sanapambaneko pa masewero anayi omwe asewera mu mpikisanowu.
Wanderers ikumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa masewero otsegulira mpira wa chaka chino pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Timuyi yasewerako masewero anayi kuchokera mu chaka cha 2015 ndipo yagonja katatu ndi Bullets ndipo kamodziko anagonja ndi Silver Strikers chaka chatha.
Iwo akukumana ndi Bullets koyamba kuchokera mu chaka cha 2023 mu mpikisanowu yomwe inawagonjetsa 2-1 komanso kuti yapambanako chikho mu chaka chilichonse chomwe asewera mu mpikisanowu.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Wanderers, MacDonald Mtetemera, wati akukonzekerabe masewerowa ndi cholinga choti adzachite bwino.
"Mbali ya nyonga za osewera tapanga ndipo tsopano tikukonza zina zomwe zatsalira kuti masewerowa tidzachite bwino komanso kuti mu ligi tidzayambe mwapamwamba," anatero Mtetemera.
Timu
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores