MITUNDU BAPTIST YAPALANA UBWENZI NDI LUANAR
Timu yomwe yangolowa kumene mu ligi yaikulu ya Mitundu Baptist yalowa mu mgwirizano ndi sukulu ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources omwe ayendere limodzi kuyambira mu ligi ya chaka chino.
Malingana ndi malipoti omwe tsamba lathu lapeza, mbali ziwirizi zamvana chilichonse ndipo mwambo wotsimikizira ubalewu uliko lamulungu pa 19 April 2026 ku Hotela ya Malville Botique.
Pa mwambowu timuyi ikaonetsa akuluakulu omwe aziyendetsa timuyi omwe ndi ochokera ku mbali zonse ziwirizi, kukhazikitsa kuti timuyi iyende ngati kampani komanso kuonetsa zovala za chaka chino.
Pa mgwirizanowu, timu ya LUANAR FC tsopano ikhala yachisodzera ya timuyi ndipo akhazikitsanso timu ya mpira wamiyendo ya amayi pokwanilitsa zoyenereza kusewera mu ligi yaikulu.
Timuyi ikuyembekezeka kusintha dzina kukhala LUANAR Mitundu FC ndipo isewera mu chaka chake choyamba mu ligi yaikulu ya mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores