BULLETS YATENGA OSEWERA AWIRI KU NTCHISI SELECT
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yatenga osewera awiri kutimu ya Ntchisi Select yomwe anasewera nayo mu masewero awo omaliza pokonzekera ligi ya chaka chino.
Mphunzitsi watimuyi Gilbert Chirwa ndi yemwe watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti awiriwa atengedwa kamba koti ndi osewera apamwamba komanso achisodzera.
Osewerawa omwe ndi Limbitso Chimanjamanja komanso Halison Juve akatumikira timu yaing'ono ya Bullets akuwayang'ana kuti maluso awo akwere.
"Tinaonako wina amasewera kumanzere komanso wakutsogolo nde titawafunsa wina ali ndi zaka 18 wina 19 nde tiwatenga kuti apite ku timu yathu yaing'ono," anatero Chirwa.
Pa masewerowa, Bullets inapambana 5-1 pa bwalo la Champions ku Dowa ndipo tsopano akuyang'ana zamu NBS Bank Charity Shield yomwe akumane ndi Mighty Wanderers loweruka likudzali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores