"TAPANGA TIMU YABWINO KUPOSA YA CHAKA CHATHA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati akukhulupilira kuti akhala ndi timu yabwino kwambiri kuposa ya chaka chatha kamba koti apeza osewera omwe athandize timuyi kwambiri.
Iye amayankhula kutsatira kumaliza zokonzekera zawo patsogolo pa ligi ya chaka cha 2026-27 ndipo wati zokonzekera zawo zonse zayenda bwino.
Iye wati amayang'ana kugwirana kwa osewera mu timuyi zomwe waona kuti zatheka ndipo akuyembekezera kukhala ndi chaka chopambana ku timuyi.
"Tili ndi timu yabwino kuposa ya chaka chatha, tabweretsa osewera abwino omwe tizitha kusinthasintha ndikutipatsa zomwe tikufuna nde tikuyembekeza kuti tisewera mwapamwamba," anatero Chirwa.
Bullets ikuyamba ligi ya chaka chino kumathero a sabatawa pomwe akumane ndi Mighty Wanderers mu masewero amu NBS Bank Charity Shield loweruka pa bwalo la Bingu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores