"CHIMENE TIKUFUNA IFEYO CHIKUTHEKA" - MTETEMERA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, MacDonald Nginde Mtetemera, wati otsatira timuyi asadere nkhawa ndi zotsatira zawo mu masewero okonzekera ligi ya FDH Premiership poti zomwe iwo akuyang'ana kwambiri zikutheka.
Mtetemera amayankhula atatha masewero omwe anagonjetsa Bangwe All Stars 2-0 ndi zigoli za Promise Kamwendo ndi Muhammad Sulumba pa bwalo la Kamuzu lolemba masana.
Iye wati ali ndi chikhulupiliro kuti ayamba bwino mu ligi ya chaka chino kamba koti zokonzekera zawo zikuyenda molingana ndi zimene iwo amafuna.
"Mavuto omwe tikuwaona tikuwakonza ndipo tidzayamba bwino. Zinthu zimene timafuna zikutheka kwambiri ndipo tili osangalala," anatero Mtetemera.
Iye anati akuyeyetsa kuti osewera aliyense wa timuyi azikhulupilire ndi cholinga choti aliyense akhale wodalilika ku timuyi.
Mtetemera akutsogolera timuyi kutsatira kuti mphunzitsi wamkulu Bob Mpinganjira ali mdziko la Scotland kokaonjezera maphunziro a uphunzitsi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores