Zonse Lotto yaika K400 million ku Bullets
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalowa mu mgwirizano ndi timu ya Zonse Lotto yomwe ithandize timuyi kwa zaka zitatu.
Kampaniyi ikhala ikupereka ndalama zokwana K400 million ku timuyi pa nthawiyi.
Ngakhale zili chomwechi, banki ya First Capital ndiwo othandiza kochuluka kamba koti ayika ndalama zokwana K3 billion kwa zaka zitatu.
Mwambowu unachitika ku ma ofesi a timuyi usiku wa lachisanu mu mzinda wa Blantyre.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores