"TISAMANGOTHANDIZA BULLETS NDI WANDERERS" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wapempha makampani ndi akufuna kwabwino kuti akwanitsenso kufikira matimu ena osati matimu akuluakulu okhaokha.
Iye amayankhula izi lachisanu kuma ofesi a timu ya FCB Nyasa Big Bullets komwe timuyi imakasainirana ndi banki ya First Capital mu mgwirizano watsopano wokwana K3 billion.
Haiya wati makampani ochuluka amangoyang'ana matimu akuluakulu okha monga Bullets ndi Mighty Wanderers koma akhonza kupindulanso atapita ku matimu ena.
"Pali matimu angapo omwe akuvutika ndi zachuma chifukwa amadalira ndalama ya mmatumba mwa anthu. Makampani chonde tiyeni tiwathandize matimu amenewa," anatero Haiya.
Matimu akuluakuluwa amakhala ndi owathandiza odutsa anayi mu chaka chilichonse zomwe zimawathandiziranso kuti azichita bwino kwambiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores