NKHANI
Timu ya Goshen City Dedza Dynamos yalembera kalata wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Luka Bruno Milanzie, kuti saonjezeranso mgwirizano wake womwe watha tsopano ndi timuyi.
Mu kalata yomwe wasaina ndi timu maneja, Elijah Ngondo, yathokoza Milanzie kamba kotumikira timuyi ndipo amufunira zabwino pomwe ayang'ane ntchito kwina.
Ndipo Milanzie wavomera kuti walandiradi kalatayi ndipo wati sangatsutsane ndi ganizo la akuluakulu a timuyi.
Iye wathokoza timuyi pokhala naye mu zaka ziwiri ndi kumukhulupilira kuti akhonza kugwira ntchito ndipo waphunzirako zambiri kamba koti ankapitako ali ndi chitupa cha uphunzitsi cha CAF C koma wachoka ali ndi CAF B.
📷: Social media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores