KULIBE KUYESA MWAYI KU TIGERS
Timu ya Mighty Tigers yalengeza kuti ikuyamba zokonzekera zawo za ligi ya NBS Bank National Division lolemba pa 9 March 2026.
Iwo alengeza izi kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook pomwe mpira wa chaka chino wayandikira.
Ana amu mpanda akuti akuyamba zokonzekera zawo mofulumira ndi cholinga chofuna kudzabwereranso mu ligi yaikulu ya dziko lino.
Timuyi yatinso kulibe kudzayesa mwayi kwa osewera achilendo ndipo azichita kuyitana omwe apezeke ku zokonzekera zawozi.
Matiga anali imodzi mwa matimu omwe anatuluka mu ligi yaikulu chaka chatha ndipo kanali koyamba chichokereni mu 1986 ndipo anapambanako ligi mu 1989.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores