NKHANI
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chakummwera kwa dziko lino la Southern Region Football Association lasintha malo omwe aperekere mphoto za omwe achita bwino mu chaka cha 2025-26.
Mu kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu wa bungweli, Ismail Sande, yati mwambowu udzakachitikira ku Robins Park osatinso ku mudzi wa Mpira ku Chiwembe.
Mwambowu udzayamba nthawi ya 10 koloko ndi kupereka mphoto za ligi ya Sultan Concrete Division One ndipo 2 koloko masana, mwambo wa mphoto za ligi ya Thumbs Up Premier division udzayamba.
Mwambowu udzachitika lachiwiri pa 3 March 2026.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores