Ngwira akhalabe ku Dedza Dynamos
Mphunzitsi watimu ya Goshen City Dedza Dynamos, Alex Ngwira, akuyembekezeka kukhalabe kutimuyi pomwe ikukonza kumupatsa mgwirizano wa zaka ziwiri kuti aphunzitsebe timuyi.
Malingana ndi malipoti omwe tsamba lino lapeza, akuluakulu a timuyi akhutira ndi momwe Ngwira wamalizira makamaka mu chikho cha Castel ndipo akukhulupilira kuti atha kuchita bwino atapatsidwa zipangizo zonse.
Ntchito ya mphunzitsiyu inali pa mpeni pomwe Peter Mponda anasendera chifupi kukhala kutimuyi koma poti analowera ku Masters Security, timuyi iyendabe ndi Ngwira.
Iye anabwera kutimuyi kulowa mmalo mwa Andrew Bunya chaka chatha ndipo ngakhale anavutika mu ligi, wakhala woyamba kutengera timuyi mu ndime yotsiriza ya chikho ndipo akumana ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Mphunzitsiyu ndi mmodzi mwa aphunzitsi omwe amapatsidwa ulemu kwambiri mdziko muno pomwe waphunzitsakonso Mighty Wanderers.
0882410060
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores