Banki ya NBS yalengeza kuti masewero otsekera ligi ya NBS Bank National Division pakati pa Red Lions ndi Baka City ku bwalo la Balaka adzakhala awulere.
Izi zayankhulidwa ndi mkulu woona nthambi ya zamalonda ku Bankiyi, Frank Magombo womwe ati zambiri zosangalatsa zakonzedwa pa masewerowa.
"Uku kukakhala oyimba monga ma Blacks, Bwede komanso Phyzix cholinga anthu adzasangalale pomwe tikumaliza ligiyi," iye anatero.
Magombo watinso anthu omwe adzafike pa bwaloli omwe ali kale ndi akaunti ya bankiyi adzakhala alowa mu mpikisano wa tsiku lomwelo omwe anthu 50 adzapate ma K10,000 ndipo ena ma T-Shirt a bankiyi.
Ndipo kwa omwe adzafune kutsegulitsa akaunti yatsopano akuyenera kudzakhala ndi chitupa chaunzika komanso K1,000 yomwe idzakhale ya buku.
Pamapeto a zonse, Red Lions idzapatsidwa chikho ndi ndalama zokwana K15 million pokhala akatswiri ndipo matimu achiwiri ndi achitatu adzapeza K10 million ndi K5 million iliyonse.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores