BANDA AKUCHOKA KU TIGERS
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya Mighty Tigers, Kelvin Banda, akuchoka kutimuyi kutsatira kuti mgwirizano wake ukutha pa 31 December 2025.
Katswiriyu watsimikiza za nkhaniyi pomwe wathokoza timuyi pokhala naye bwino mu zaka zomwe watumikira ku ana akumpanda.
Iye wakhala wofunikira kwambiri kutimuyi pomwe amatchinga bwino kwambiri ndipo wafunidwapo ndi Civil Service United, Creck Sporting Club komanso Mighty Wanderers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores