''Padakali panopa sitinapulumuke mu ligi'' - Lungu
Mphunzitsi watimu ya Ntaja United, Mavuto Lungu, wati akuyitengabe timu yake ngati ikadalibe ku chigwa cha matimu otuluka mu NBS Bank National Division League ndipo adzasangalala akadzatsimikizika kuti apulumuka mu ligi.
Iye amayankhula kutsatira kupambana 2-1 ndi timu ya Chintheche United pa masewero omwe akanati agonja akanatuluka mu ligi koma atuluka mu chigwachi ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri.
''Tikuzitenga kuti tikadalibe komwe kuli matimu otuluka, inde tapambana koma sitinasunthe ndipo ntchito ikadalipobe yambiri nde tichilimika tidzasangalalanso tikadzatsimikizika kuti tapulumuka mu ligi,'' anatero Lungu.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu pomwe ili ndi mapointsi okwana 26 pa masewero 21 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores