''Takhumudwa ndi kayimbilidwe pa masewerowa'' - Kayuni
Mphunzitsi watimu ya Chintheche United, Kaloti Kayuni, wati ndi wokhumudwa ndi penate yomwe oyimbira anapereka ku timu ya Ntaja United kamba koti palibe yemwe anagwetsedwa kapenz kugundidwa.
Iye amayankhula atagonja 2-1 ndi timu ya Ntaja United pa bwalo la Balaka ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri koma penateyo yawapweteka pa masewerowa.
''Tinapeza mipata yochuluka mu chigawo choyamba koma tinakanika kugoletsa ndipo mchigawo chachiwiri tinapeza chigoli komano oyimbira anapereka penate yomwe palibe anagundidwa ndipo takhumudwa ndi kayimbilidwe ka mmasewerowa,'' anatero Kayuni.
Iye wati timu yake ikadali ndi mwayi wotsalira mu ligi ndipo mu masewero awo omaliza ndi timu ya FOMO adzachilimika kuti adzachitd bwino.
Timuyi ili pa nambala 9 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 25 pa masewero 21 omwe asewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores