''NDATULA PANSI CHIFUKWA NDASAUKA'' - CHIPANGA
Yemwe anali wapampando kutimu ya Karonga United, Alufeyo Chipanga, watsimikiza kuti watula pansi udindo wake kutimuyi chifukwa choti wasauka.
Iye amayankhula kutsatira malipoti omwe anazungulira kuti iye watula pansi udindo ndipo wati malinganadi ndi kanema yemwe anazungulira pa masamba a mchezo omwe ochemerera amamunena kuti wasauka ndithu ndi zoonadi.
Iye watinso ndi zoonadi kuti timuyidi siyaku Mchinji ndipo sangakwanitsenso kuthandiza timuyi kumbali ya za chuma koma upangiri wina kamba koti wasauka.
''Ndi zoonadi kuti ndatula pansi udindo ndipo chifukwa chake ndi chakuti ndasauka,'' anatero Chipanga.
Iye wati ndi wampira ndipo ndi okonzeka kugwira ntchito ndi timu iliyonse koma osati ku mbali yazachuma kamba koti iwo asauka.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores