''Mwayi ukadalipo wambiri kwa ife'' - Kajawa
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Trevor Kajawa, wati timu yake ikadalibe ndi mwayi woti atsale mu TNM Supa ligi ndipo wati alimbikira mu masewero omwe atsala nawo kuti achite bwino.
Iye amayankhula atagonja 3-0 ndi timu ya Mighty Tigers ndipo wati timu yake inapereketsa chabe zigoli zophweka mu chigawo chachiwiri zomwe zathandizira kuti agonje.
Iye wati osewera ake ndi omwewa omwe anakhala masewero asanu osagonjako mu ligi ndipo akukhulupilira kuti atsalirabe mu ligi.
''Mwayi ukadalipobe wochuluka kwambiri ndipo tikungofunikira kuti tichilimike mu masewero atsalawa zikatero tidzatsala mu ligi,'' anatero Kajawa.
Timuyi ikadali pa nambala 13 mu ligiyi pomwe ili ndi mapoints okwana 26 pa zipambano zisanu ndi chimodzi, kulepherana kasanu ndi katatu ndi kugonja kakhumi ndi kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores