NKHANI
Mphunzitsi watimu ya mpira wamiyendo koma ali amayi ya dziko lino, Lovemore Fazili, akuyembekezeka kutulutsa ndandanda wa osewera omwe agwiritse ntchito mu mpikisano wa matimu atatu omwe uyambe kumathero a mwezi uno.
Fazili akuyembekezeka kuulutsa ndandandawu ku mmawa kwa lero kuyambira 9:30.
Mpikisanowu omwe matimu a Zambia ndi Zimbabwe akhale akutenga nawo mbali wakonzedwa ngati mbali imodzi yomwe timuyi ikhale ikukonzekera chikho cha mayiko amu Africa muno cha WAFCON.
Nkhani yabwino ndi yakuti katswiri Tabitha Chawinga adzapezeka nawo pa mpikisanowu koma Temwa Chawinga akadali okayikitsa ngakhale ali kopumulira ligi chifukwa anavulala.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores