''Oyimbira achepetse kukondera matimu'' - Chimkwita
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Chrispin Chimkwita, wati oyimbira atengapo mbali kuti timu yake igonje ndi timu ya Creck Sporting Club ndipo wati izi zikulowetsa mpira pansi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Aubrey Dimba ndipo wati ziganizo za oyimbira zimachita kuonekeratu kuti amafuna kuti iwo agonje mmasewerowa.
''Awa oyimbirawa asamakhald ndi mbali, ilinso si vuto la oyendetsa koma oyimbira eni ake akumachita kuoneka kuti akufuna kuti timu igonje nde zimenezi sizabwino ayi zikuononga mpira wathu,'' anatero Chimkwita.
Mmasewerowa, Lovemore Ngolombe komanso mphunzitsi wamkulu Oscar Kaunda analandira ma kadi ofiyira ndipo Ramadan Ntafu anagoletsera Creck.
Karonga ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 37 pa zipambano 11, kufanana mphamvu kanayi ndi kugonja kasanu ndi katatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores