Mphunzitsi wa Jenda amafuna kulowa m'bwalo kuti asewere
Zinthu zafika povuta kutimu ya Jenda United pomwe mphunzitsi watimuyi, Uchizi Nkunika, amafuna alowe pa masewero omwe timuyi imasewera ndi Baka City mu NBS Bank National Division League kamba kosowa osewera.
Timuyi inali ndi osewera mmodzi yekha panja ndipo atasintha, osewera wina anavulala zomwe zinachititsa mphunzitsiyu kufuna kulowa yekha.
''Ndikanatha kulowa ndithu mpira ndasewerapo ndipo ndikadali ndi mphamvunso mwinanso ndikanatha kugoletsanso nanga tinalibe osewera wina. Ndimavuto omwe tili nawo kutimuyi omwe sindingakambe poti nditha kuyivula timuyi,'' anatero Nkunika.
Masewerowa anakomera timu ya Baka City 2-0 kupangitsa kuti Jenda ikhale pafupifupi kutuluka mu ligiyi pomwe manambala sakuwalolanso kuti atha kupulumuka mu ligi.
Timuyi ili pansi ndi mapointsi asanu pa masewero 17 pomwe yapambana kamodzi, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja ka 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores