Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya Karonga United, Alfred Chizinga, sapezeka kwa ma sabata anayi pomwe ndi wovulala.
Timuyi yatsimikiza za izi kudzera pa tsamba lake la mchezo la Facebook kuti katswiriyu wavulala ku zokonzekera za timuyi ndipo madotolo amuuza kuti apume kaye kwa sabata zinayi.
Chizinga amadziwika bwino ndi khalidwe lake lozinga matimu akulu-akulu pomwe amakonda kuyikhaulitsa Mighty Wanderers ndipo anagoletsa chigoli chofunikira kwambiri pomwe Karonga United inalepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets 3-3.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores