FAM yaimitsa zikho zina chifukwa cha chisankho
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti mpikisano yonse yomwe imayendetsedwa pansi pa bungweli yayimitsidwa kale chifukwa cha chisankho.
Mu kalata yomwe bungweli latulutsa yati kuyambira pa 12 September mpaka pa 18 September ma ligiwa sapitilira kamba koti ena amu zikhozi akukhudzidwa nawo pa chisankho cha pa 16 September chomwe Malawi idzakhale ikusankha mtsogoleri wa dziko, a phungu a nyumba ya malamulo ndi ma khansala.
Ena mwa mpikisano yomwe ikukhudzidwa ndi ya NBS Bank National Division League komanso wa National Bank of Malawi National Women's Premiership.
FAM yati masewero adzabwereranso mchimake pa 19 September 2025 pomwe mpikisanoyi ikudzayambiranso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores