Zitha ikuyang'ana zolowa mu Supa ligi chaka cha mawa
Timu ya Namitete Zitha tati yaika chidwi chachikulu kuti azichita bwino mu ligi ya NBS Bank National Division pomwe akufunitsitsa kulowa mu supa ligi chaka cha mawa.
Izi zanenedwa ndi mphunzitsi watimuyi, Richard Fosiko, pomwe anachokera kumbuyo lamulungu kuti afanane mphamvu 2-2 ndi timu ya Chilumba Barracks pa bwalo la Karonga.
Iye anati timu yawo ikuchilimika kwambiri pomwe akufunitsitsa kuti adzathere pa nambala yoyamba mu ligiyi cholinga chaka cha mawa adzamenye mu supa ligi.
"Maso athu tayika pa Supa ligi chaka chas mawa chifukwa chake tikulimbikira kuti mwina tithere kumtundako koposaposa pa nambala 1 nde tiwalimbikitsebe osewerawa kuti tipitilire kuchita bwino." Iye Anafotokoza.
Timuyi yasewera masewero asanu ndi amodzi (6) pomwe yapambana katatu, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja kamodzi ndipo ali ndi mapointsi okwana 11 pa nambala yachinayi (4) mu ligiyi.
Wolemba : Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores