"Oyimbira akumatigwetsa ulesi" - Mpinganjira
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati oyimbira pa masewero awo ndi Silver Strikers sanali bwino pomwe mbali zonse zimamudandaula ndipo azitolere pork matimu amaononga zambiri pa masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Silver pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira anyamata ake momwe anachitira koma analoza chala oyimbira kuti ntchito sanagwire bwino.
"Pachigoli paja chinnaoneko chimene anayimba komanso kuchokera pachiyambi mbali zonse zimamudandaula nde izizi zimagwetsa ulesi chifukwa timakhala tataya mphamvu zathu pachabe." Anafotokoza.
Iye koma wati osewera atimuyi atenga mbali yabwino pomwe tsopano akuoneka kuti akusewera bwino kwambiri.
Timuyi tsopano ikadali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi ma points 13 pa masewero asanu omwe asewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores