"Dabe sitengera kuti alibwino ndi ndani" - Mponda
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Mponda, wati kupambana kwawo ndi Kamuzu Barracks 4-0 sikopereka mangolomera patsogolo pa masewero awo ndi Mighty Wanderers Sabata ya mawa poti masewero ake samatengera kuti alibwino ndi uti.
Iye amayankhula atatha masewerowa loweruka pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira osewera ake kuti anachita bwino komanso kuti akukwanitsa kuchita bwino akamasewera mmalo osiyanasiyana.
Iye anatinso masewero awo ndi Wanderers ndi osiyana ndi onse ndipo ayambe zokonzekera zake mkati mwa sabatayi.
"Amenewo ndi masewero osiyana samatengera kuti alibwino ndi ndani nde kwa lero tingosangalala kuti tapambana kenako tiyambe zokonzekera zathu mkati mwa Sabata ikudzayi." Iye anatero.
Timu ya Bullets ili ndi mapointsi 18 mu Ligi pomwe yakwanitsa kupambana masewero onse asanu ndi amodzi ndipo akadali pamtunda pa Ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores