NKHANI
Bungwe la Confederations of African Football lalamula kuti masewero apakati pa Cameroon komanso Kenya omwe anaseweredwa pa 16 October 2024 amu ndime yopitira ku African Cup of Nations aseweredwenso.
Bungweli lati lachita izi kamba koti panali zinthu zolakwika zochuluka zomwe zikukhudzananso ndi zachinyengo zomwe zinathandiza Cameroon kupambana 4-1.
Ilo lati masewerowa aseweredwe pasanathe masiku 60, adzaseweredwe pa bwalo loti timu iliyonse idzakhale koyenda, goloboyi wa Kenya, Patrick Matasi ndi osewera ena akuwafufuza ndipo akapezeka olakwa akhale akupatsidwa zilango zomwe zifike pa kusadzaseweranso mpira mmoyo wawo onse komanso ndalama za pa masewerowa apereke ndi a CAF.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores