FAM INDIPATSE K157 MITA-MABEDI
Patrick Mabedi yemwe anachotsedwa ntchito ngati Mphunzitsi wa timu yadziko lino ya Malawi the Flames, watengera bungwe oyendetsa Mpira mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM) ku bwalo la milandu ati kamba komuchotsa ntchito mosatsata ndondomeko.
Kudzera mwa omwe akuimira Mabedi pa mlandu wu a Makiyi Kanyenda Associates ati a Mabedi akufuna chipepeso maka kamba kakuti bungwe la FAM linawachotsa ntchito mosatsata ndondomeko zoyenera ndipo ichi mchifukwa chake atengera nkhani yi ku bwalo la milandu.
Bungwe la FAM linachotsa ntchito a Mabedi kamba kakuti timu ya dziko lino ya Mpira wa miyendo yakhala isakuchita bwino pa masewero ake olimbirana malo opita ku African Cup of the Nations omwe ukasewereddwe ku Morocco chaka cha mawa.
Malawi the Flames inagonjetsa masewero ake onse anayi oyambilira ku matimu monga Burkina Faso, Burundi komaso Senegal kawiri konse.
Ngati bungwe la FAM lingapezeke lolakwa pa nkhani yi ndiye kuti likuyenera kuwalipir
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores