"OYIMBIRA AKUFUNA KUPULUMUTSA TIMU YAKUMMWERA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati timu ya Bangwe All Stars inasamuka dala ku Blantyre kuti izikapanga masamu ndi oyimbira ku Balaka pomwe wati mpira tsopano walowa mu zigawo tsopano.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Balaka ndi chigoli chakumapetopeto ndipo wati amadziwadi kuti oyimbira akhale akukondera Bangwe kuti ipambane mmasewerowa.
"Anali masewero ophweka kwambiri koma mpirawu walowa mzigawo tsopano akuyesetsa kupulumutsa timu yakummwera nde mwaona lero atikanira chigoli chabwinobwino ndi ziganizo zina zabodza, timadziwa kuti zivuta ndithu komabe tapilira mpaka kumapeto tachinyitsa." Anatero Makawa.
Timu ya Civil Service United ikadali pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 39 pa masewero 27 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores