APHUNZITSI AKHUTIRA NDI FLAMES
Wachiwiri kwa mphunzitsi wogwirizira kutimu ya Flames, Peter Mponda, wati kulepherana 0-0 ndi timu ya Burundi koyenda ndi poyambira pabwino ndipo akhutira ndi mmene osewera anachilimikira pa masewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana ndi Burundi ku Ivory Coast ndipo wati ngakhale kaseweredwe sikanali bwino, iwo akulimba mtima kuti akhale akukonza timu yabwino.
"Kufanana mphamvu komanso koyenda ndi poyambira pabwino anyamata ationetsa mphamvu kwambiri analimbikira chabwino kaseweredwe sikanali kabwino poti nthawi yokonzekera inali yochepa kwambiri koma atilimbitsa mtima kuti tipanga timu yabwino." Anatero Mponda.
Pa masewerowa, timuyi inakhulupilira ankhalakale ngati Gabadinho Gabadinho Mhango ndi Richard Mbulu kutsogolo kwa timuyi koma pa mipira yomwe anayesa pagolo kasanu ndi kawiri palibe wafikako pagolo.
Masewero otsatira ali pakati pa timuyi ndi Burkina Faso pa masewero omwe adzaseweredwa lolemba pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Li
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores