"TASANGALALA NDI KUBWERA KWA GABA, MBULU NDI PETRO" - BANDA
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya Flames, John Banda, wati kubwera kwa osewera ena monga Gabadinho Mhango, Richard Mbulu ndi Charles Petro komanso osewera ena atsopano ndi kwabwino kwambiri pomwe kuwathandize kuti apeze chipambano.
Banda amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe akumane ndi Burundi ku Ivory Coast lachinayi ndipo wati osewerawa ndi odziwika kuti apamwamba ndipo awathandiza kupezako chipambano mu gulu lawo.
Iye watinso masewerowa ndi ofunikira kwambiri kutimuyi pomwe akhala okhaokha opanda kupeza chipambano ndipo ayesetsa kuti apambane mmasewerowa komanso kuti sanganamizire kuchepa Kwa nthawi yokonzekera.
"Zonse zilibwino ndipo takonzekera kwambiri ngakhale kuti nthawi yathu yokonzekera inali yochepa kwambiri koma sitinganamizire zimenezo chifukwa ntchito yathu ndi kusewera mpira." Anatero Banda.
Malawi ili ndi ntchito yongomalizitsa chabe masewero opitira ku African Cup of Nations pomwe iwo anakanika kale p
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores