"TAPEREKETSA CHIGOLI CHA MSANGA" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Elvis Kafoteka, wati timu yake yagonja kamba koti anapereketsa chigoli mwa msanga komanso kuti amasewera ndi timu yabwino koma wayamikira osewera ake kamba kosewera mwapamwamba.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo wati anyamata ake sanadzuke bwino chabe.
"Anali masewero abwino, analinso masewero ovuta kwambiri kutengera kuti timasewera ndi timu yabwino, tapereketsa chigoli cha msanga koma kupanda kutero mwina bwenzi tikuti tafananitsa mphamvu kapena tapambana kumene koma tiwayamikire kuti asewera bwino." Anatero Kafoteka.
Iye wati timu yake ikuyang'ana masewero aliwonse ndi chidwi ndipo awonetsetsa kuti achite kuti atsalirebe mu ligi.
Timuyi ikadali pa nambala 13 mu ligi pomwe tsopano ili ndi mapointsi okwana 22 pa masewero 22 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores