CIVIL YAFIKA PA NAMBALA YACHISANU
Timu ya Civil Service United yasuntha pa ndandanda wa matimu mu ligi ya TNM pomwe tsopano yafika pa nambala yachisanu mu ligi kutsatira kulepherana 0-0 ndi timu ya MAFCO FC pa bwalo la Civo lachitatu.
Timuyi inali ndi mipata yochuluka yoti ikanatha kugoletsa makamaka mchigawo chachiwiri koma anyamata awo Christopher Gototo ndi Muhammad Biason analephera kuti agoletse mipatayi.
Mphunzitsi watimuyi, Abbas Makawa, anavomereza kuti timu yake sinasewere bwino mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta kwambiri, sitinayambe bwino nde timayesa kuti anyamata mwina azitolera mphindi zikamapitabe koma tivomereze kuti sitinasewere bwino. Tinali ndi mipata ingapo yoti tikanatha kupeza zigoli koma taphonya ndithu, tiyang'anabe chitsogolo." Anatero Makawa.
Timuyi tsopano ili ndi mapointsi okwana 28 pa masewero 20 omwe yasewera ndipo yadumpha manambala atatu kuti ifike pa nambala yachisanu mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores