"ENA ATI NDIFE 4 BY 4, TIMASEWERA NDI GOLOBOYI WA MAFCO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati sanali odabwa kuona kuti Christopher Mikuwa anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba pa masewero awo poti timu yawo imasewera ndi iyeyo.
Nyambose amayankhula atatha masewero omwe timuyi yafanana mphamvu 0-0 ndi MAFCO ndipo wati amadziwa kuti MAFCO ibwera movuta poti iwo akumagawa zigoli zinayi.
"Sizodandaulitsa taonjezera point imodzi pamenepo tiwayamikire anyamata asewera mpira wathu changovuta kuti tigwetseremo koma timadziwa kuti MAFCO sibwera mophweka chifukwa ena akumatitcha Mr 4, ena 4 by 4 chifukwa tikumagawa zigoli zinayi nde iwo anali kale akudziwa." Anatero Nyambose.
Iye wati timu yake ikadalipo mpaka kale ndipo chaka cha mawa iseweranso mu ligi ya TNM chifukwa situluka.
Chitipa ikadali pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi okwana 16 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores