"TIYESETSA KUTI TIPAMBANEKO KOYENDA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake iyesetsa kulimbikira kuti mwina ipezeko chipambano chawo choyamba koyenda pomwe wati kuti atsale mu ligi akufunika kumapambana masewero.
Iye wayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mighty Tigers onwe aliko loweruka pa bwalo la Mpira ndipo wati wawalimbikitsa kuti achite bwino ngakhale kuti akukumana ndi timu inanso yabwino.
"Zokonzekera zathu zayenda bwino ndipo anyamata akuoneka kuti akuchita bwino ndipo tikuyesetsa kuti tikachite bwino poti anthu akutinena kuti sitikumawina koyenda koma tikuwalimbikitsa anyamatawa kuti tsiku lina adzapambanako nde Tigers ndi timu yabwino koma tiyesetsa." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO ili pa nambala 13 mu ligi pomwe yakwanitsa kutolera mapointsi okwana 14 pa masewero 14 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores