BANGWE YAMANG'ALA KU SULOM
Timu ya Bangwe All Stars yalembera bungwe la Super League of Malawi kudandaula ndi ziganizo zomwe oyimbira, Rose Zimba, anapereka pomwe timuyi inalepherana 1-1 ndi Moyale Barracks.
Mu Kalata yomwe yasainidwa ndi mkulu woyendetsa ntchito za timuyi, Steve Palemeza, yati oyimbirayu wachita zambiri zomwe zinali zokondera timu ya Moyale.
Iyo yati Zimba anapereka kadi yofiira kwa osewera wawo pomwe panalibe chifukwa chenicheni ndipo amangogawa makadi achikasu kwa osewera akadandaula kwa iye komanso kuti anapereka penate yabodza kwa Moyale kuti ibwenze.
Timuyi yati ikufunitsitsa kuti chilungamo chioneke ndipo ikuyembekezera kuti SULOM ichitapo kanthu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores