RAMADAN WAPEZA NTCHITO KU TANZANIA
Mphunzitsi wakale watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Nsanzurwimo Ramadan, waikidwa kukhala wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Singida Fountain Gate yomwe imasewera mu ligi ya mdziko la Tanzania.
Izi zadziwika lachisanu pomwe timuyi yalengeza za nkhaniyi pa tsamba lawo la mchezo la Facebook.
Ramadan wapeza ntchito patatha masabata atatu atalengeza kuti wasiya ntchito ku timu ya Wanderers atangothako masabata asanu ndi anayi (9) basi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores