"NDALAMA YAKE NDI YABWINO" - RAPSON
Osewera wakale watimu ya Blue Eagles, Richard Rapson, wati ndalama yomwe akulandira ku timu ya Desportivo de Nacala ndi yabwino kusiyana ndi yomwe amalandira ku Malawi kuno.
Katswiriyu wauza Owinna kuti umoyo wake ku Mozambique ukuyenda bwino kwambiri pomwe akulandira ndalama pafupifupi K700,000 komanso kuti timuyo ikumukonda kwambiri.
"Kunoko kulibwino kwambiri komanso ndalama yake ndikayisintha ikumafika K700,000 nde aah ndi yamphamvu." Anatero Rapson.
Katswiriyu anachoka kutimu ya Blue Eagles mgwirizano wake utatha ndiponso kutuluka kwa timuyi mu ligi kunachititsa iye kusaonjezera mgwirizano wake.
Iye wasewera matimu a Hangover, Mighty Mukuru Wanderers, Ntopwa, Ekwendeni Hammers komanso Blue Eagles mu dziko lino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores