MAOFESI A FAM AKUSAMUKIRA KU LILONGWE
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi (FAM), Fleetwood Haiya, wati ma ofesi a bungweli akhale akusamuka kuchoka ku Blantyre ku Mpira house kupita mu mzinda wa Lilongwe.
Haiya wafotokoza za nkhaniyi lachinayi ku Lilongwe pomwe amakumana ndi mtsogoleri wa bungwe la FIFA, Gianni Infantino, ndipo wati posachedwapa akhale akutero.
Ndipo Infantino wavomera za ganizoli ndipo wati bungwe lake ndi lokonzeka kuthandiza ntchito yomanga ma ofesiwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores