"SITINAKUYIWALE MABEDI" - AMALAWI
Anthu okonda mpira wamiyendo mdziko muno ati sikuti ayiwala za kugonja kwa Flames ndi Equatorial Guinea sabata yapitayo ndipo ayikambabe akamaliza kukhudza maliro a yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Klaus Chilima.
Anthuwa aoneka ndi ndemanga zosiyanasiyana pa tsamba la mchezo la Facebook pomwe ati Patrick Mabedi asaone ngati anthu sanaone mmene timu inachitira pomwe inangomenyerako pagolo kamodzi mmasewerowa.
Timu ya Flames inaphonyana ndi mwayi ofika pa nambala yachiwiri mu gulu lawo kutsatira kugonjaku pomwe tsopano akutsalira ndi ma points anayi kuti ayipeze Tunisia yomwe ili pa nambala yoyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores