SULOM YATSEGULA MILANDU IWIRI KU BULLETS
Bungwe la Super League of Malawi, SULOM, latsegula milandu iwiri kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets kutsatira zipolowe zomwe zinachitika pomwe timuyi imasewera ndi Silver Strikers lamulungu lapitali.
Bungweli lati Bullets ili ndi mlandu wokanika kuletsa ochemerera atimuyi kuchita zipolowe pa masewero a mpira wa miyendo komanso wobweretsa chisokonezo pa masewero ampira.
Bungweli lapereka maola 48 kuti timuyi ivomere kapena kukana milanduyi kenako chigamulo chidzatsatira pa nkhaniyi.
Zipolowezi zinayamba pomwe timu ya Silver Strikers inagoletsa chigoli pa mphindi 90 za masewerowa ndipo miyala ndi mabotolo zinaponyedwa komanso kugendedwa ndi kubooledwa kwa ma bus a matimu awiriwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores