"NDASANGALALA POPAMBANA KOYENDA KOYAMBA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yapeza chipambano chawo choyamba koyenda ndipo wayamikira osewera ake potsatira zomwe anauzidwa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya MAFCO 2-1 loweruka pa bwalo la Chitowe ndipo wati anadziwa kuti alowetse anyamata osunga mpira mchigawo chachiwiri ndipo ndi omwe agoletsanso.
"Ndine osangalala kwambiri poti tapambana koyamba koyenda ndipo tiwayamikire anyamata kamba kolimbikira mpaka tapambana, zomwe tinawauza anachita nde ndine wosangalala. Timadziwa kuti tilowetse anyamata osunga mpira nde zinagwira ndipo onsenso agoletsa." Anatero Mtetemera.
Mphunzitsiyu watsala kuti apeze mapointsi anayi okha pa omwe anapatsidwa kuti apeze pa masewero atatu akutsogoloku ngati akufuna asunge ntchito yake.
Kutsatira kupambanaku, Iwo ali pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 14 pa masewero asanu ndi anayi (9) mu l
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores