"FOMO TSOPANO IMENYA MATIMU" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO, Gilbert Chirwa, wati kwa nthawi yoyamba waona timu yake ikusewera mwapamwamba ndipo tsopano ikhale ikulanga matimu ochuluka mu ligiyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mzuzu City Hammers ,2-1 pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati timu yake yayamba kulimbitsa mtima kuti apeza yokhazikika yoti ichite bwino.
"Anali masewero abwino kwambiri ndipo tapambana, mwina kwa nthawi yoyamba ndaona timu yolimbitsa mtima kuchoka pachiyambi mpaka kumapeto nde mwina mmene takhala tikuchitira mu zokonzekera zathu timabwerera mmbuyomu kuwaphunzitsa koma tsopano ikuoneka ilibwino ndipo imenya matimu." Anatero Chirwa.
Iye wati oyimbira mmasewerowa anapereka penate yabodza mmasewerowa komanso ziganizo zina zinali zabodzazo koma zabwino poti awina.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) ndi mapointsi Khumi (10) pa masewero asanu ndi anayi pomwe yapambana katatu kufanana mphamvu kamodzi ndi kugonja kasanu (5)
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores