FOMO YATENGA HARRY NYIRENDA
Timu ya FOMO FC yatenga katswiri wotseka kumbuyo wakale watimu ya Flames komanso Mighty Mukuru Wanderers, Harry Nyirenda, kuti awathandizire kutseka kumbuyo kwa timuyi mu ligi.
Mphunzitsi watimuyi, Gilbert Chirwa, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati ukadaulo wake upindulira timuyi ndi osewera ena achisodzera kuti ayende bwino mu ligi.
"Tinaganiza zomutenga kuti atithandizire mavuto ena ndi ena kumbuyoko nde akungofunikira azitolere mphamvu koma ndi chiyamba kale ukadaulo ali nawo." Anatero Chirwa.
Patsogolo pa masewero awo ndi Mzuzu City Hammers, Chirwa wati iwo awunikira mavuto awo onse omwe anali nawo ndi timu ya MAFCO ndipo awauza mmene angagonjetsere timuyi.
Chirwa waphunzitsanso Nyirenda ku timu ya Mzuzu City Hammers limodzi ndi wachiwiri wake, Luckson Mauluka Nyoni ndipo aka kakhale kachiwiri kugwirira ntchito limodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores