"TIKANATHA KUPEZA ZIGOLI 8" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wadandaula ndi mmene timu yake yachitira ngakhale kuti yapambana poti wati yaphonya kwambiri pa masewero awo ndi Baka City.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Baka City 3-0 pa bwalo la Civo ndipo wati akanatha kufikitsa zigoli zisanu ndi zitatu (8) akanakhala kuti anagwiritsa ntchito mipata yawo.
"Zoonadi tasangalala poti tapambana masewerowa ndi zigoli zitatu, kungoti tadandaula poti taphonya mipata yochuluka yoti ikanatha kukhala zigoli mwina 8 koma basi chanzeru tatenga ma pointsi atatu." Anatero Makawa.
Kutsatira kupambanaku, timuyi ili tsopano pa nambala yachisanu ndi mapointsi Khumi ndi anayi (14) pa masewero asanu ndi anayi (9).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores