"TIKANGOKWANITSA KUGOLETSA ZIYAMBA KUYENDA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake ikuonetsa zizindikiro zoti posachedwa ikhale yabwino kamba koti osewera ake achisodzera akadakhazikikabe mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi Kamuzu Barracks ndipo wati kuchinyitsa mofulumira ndi kuphonya ndi zomwe zachititsa kuti agonje.
Iye wati abwerera kukakonza mavuto awo onse ndikuti achite bwino pa masewero awo omwe ali mkudza.
"Tikangodziwa poyika mpira mu ukonde zinthu ziyamba kuyenda bwino, ndine wokondwa ndi mmene akusewerera nde ambiriwa ndi ana oti amamenya SIMAMA nde akadaphunzira, tikhala ndi timu yabwino." Anatero Kaunda.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) pomwe ali ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores