"TIMAFUNITSITSA TITAPAMBANA MMASEWEROWA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati siwokondwa ndi mmene timu yake yachitira pa masewero ake ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati iye amafunitsitsa atapambana masewerowa.
Iye anayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Bullets 0-0 pa bwalo la Mzuzu masana a lolemba ndipo wati anyamata ake aphonya mipata yochuluka yomwe ikanatha kuwathandiza.
"Sindinasangalale ndi mmene zathera chifukwa timafunitsitsa kupambana ndipo tinayesetsa koma mwaona taphonya kwambiri lero zomwe si zinthu zabwino nde koma tikonza molakwikamo kuti masewero omwe timenye ndi Tigers tipambane." Anatero Mwansa.
Timu ya Moyale Barracks ili pa nambala 7 ndi mapointsi khumi ndi imodzi (11) pa masewero asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores