APHUNZITSI A CHITIPA ATSANZIKA
Aphunzitsi atimu ya Chitipa United, Macnerbert Kadzuwa komanso Elvis Kafoteka atsanzika kutimuyi pomwe ati ayesera kuti asinthe zinthu koma zikuoneka zikuvuta.
Mlembi wamkulu wa timuyi, Watson Kabaghe, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati wafunira zabwino aphunzitsiwa ndikuwathokoza kamba kokhala ndi timuyi.
Ndipo Kafoteka wati chiganizochi chabwera ndi cholinga chofuna kuti ena ayesenso mwayi wobweretsa zipambano kutimuyi.
"Kutengera ndi mmene timuyi imachitira chaka chatha, ifeyo tinayesetsa kuti mwina tibwererenso koma zikuoneka zikuvuta nde mwina ena akhonza kudzasinthako zinthu." Anatero Kafoteka.
Awiriwa ayisiya timuyi ili pa nambala 14 ndi mapointsi asanu (5) pa masewero asanu ndi atatu (8) ndipo apambana kamodzi, kugonja kasanu ndi kufanana mphamvu kawiri
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores