"ANYAMATA ANATSATIRA ZOMWE ANAUZIDWA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati ndi wokondwa kamba koti apeza chipambano ku Blantyre ndipo wayamikira osewera ake kuti anatsatira zomwe iye amawauza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Waka Waka Tigers 3-2 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akufunika awauze anyamata ake kuti azilimbikira mpaka pamapeto poti Tigers ikanatha kubwenza.
"Ndife okondwa kwambiri poti tapambana ndipo tiwathokoze anyamata poti anatsatira zomwe anauzidwa nde tinakwanitsa kupeza mipata tagoletsa, ndife osangalala." Anatero Kamanga.
Iye anati kuvulala kwa katswiri wawo Sam Gunda sikunasokoneze kalikonse pomwe analowetsa Patrick Banda yemwe anagwiranso ntchito yapamwamba.
Kutsatira kupambanaku, timuyi yafika pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 15 pa masewero asanu ndi atatu (8) omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores