"TIKUYESETSA KUTI ZINTHU ZIKHALE BWINO" - SUZUMILE
Mmodzi mwa aphunzitsi kutimu ya Bangwe All Stars, White Suzumile, wati anthu onse kutimuyi akuyesetsa kuti achite bwino koma zinthu zikuvuta poti pali zambiri zomwe zikuchitika kutimuyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Dedza Dynamos pa bwalo la Dedza ndipo wati timu yake ikanika kuchinga mipira yammwamba yomwe Dedza Dynamos imaika mkati.
"Anali masewero abwino bwino koma takanika kutchinga mipira ya mmwamba yomwe anzathuwa amayika komabe sikuti tasewera moipa koma kungoti zinthu zikuvuta ndipo masapota sangazione poti kukuchitika zambiri koma tikuyesetsa kuti ziyambenso kuyenda." Anatero Suzumile.
Timuyi ikusakasaka chipambano chawo choyamba mu ligi ya chaka chino pomwe tsopano yagonja kasanu ndi kufanana mphamvu katatu ndipo ali ndi mapointsi atatu pa nambala 15.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores