"TAKONDWA POTI TAPEZA CHIPAMBANO" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati ndi wokondwa kamba kopambana masewero awo ndipo wayamikira osewera Ake kuti anachita bwino kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Bangwe All Stars 3-0 ndipo wati wasangalala poti anakwanitsa kupeza mipata yochuluka ndi kugoletsa zigoli zitatu.
"Anali masewero abwino ndipo timakumana ndi timu yabwino, Bangwe yatipatsa masewero abwino chifukwa nthawi zina timataya mipira koma titagoletsa tinayamba kusewera bwino ndipo tinapeza mipata yochuluka komanso anyamata analimbikira." Anatero Bunya.
Timu ya Dedza Dynamos tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi imodzi (11) pa masewero asanu ndi atatu (8) per yapambana kawiri, kugonja kamodzi ndi kufanana mphamvu kasanu (5).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores